-
1 Samueli 14:32, 33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Zitatero, anthuwo anayamba kuthamangira zinthu za adani awowo mosusuka ndipo anatenga nkhosa, ngʼombe ndi ana a ngʼombe. Ankaziphera pansi ndipo ankadya nyamayo pamodzi ndi magazi ake.+ 33 Ndiyeno anthu ena anauza Sauli kuti: “Anthutu akuchimwira Yehova. Akudya nyama pamodzi ndi magazi ake.”+ Iye anati: “Mwachita zinthu mopanda chikhulupiriro. Gubuduzani chimwala mubwere nacho kuno mwamsanga.”
-