-
Levitiko 23:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata, pamene munabweretsa mtolo kuti ukhale nsembe yoyendetsa uku ndi uku,+ muziwerenga masabata 7, ndipo sabata iliyonse izikhala ndi masiku okwanira. 16 Muziwerenga masiku 50+ kukafika pa tsiku lotsatizana ndi tsiku limene Sabata la 7 lathera, kenako muzipereka nsembe yambewu zatsopano kwa Yehova.+
-