-
Numeri 28:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Imeneyi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku imene ndinakulamulani kuphiri la Sinai. Ndinakulamulani kuti muziipereka kwa Yehova kuti ikhale nsembe yakafungo kosangalatsa,* yowotcha pamoto. 7 Muziipereka pamodzi ndi nsembe yachakumwa chokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini. Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense+ muzipereka nsembe yachakumwa. Muzithirira Yehova nsembe yachakumwa choledzeretsa mʼmalo oyera.
-