Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Komanso muzichita Chikondwerero cha Zokolola.* Muzikondwerera zipatso zoyamba kucha za mbewu zimene munadzala mʼminda yanu, yomwe ndi ntchito ya manja anu.+ Muzichitanso Chikondwerero cha Kututa* kumapeto kwa chaka, mukamatuta zipatso zamʼmunda, yomwe ndi ntchito ya manja anu.+

  • Levitiko 23:34-36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Tsiku la 15 la mwezi wa 7 umenewu, ndi tsiku lochitira Yehova Chikondwerero cha Misasa kwa masiku 7.+ 35 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. 36 Kwa masiku 7 muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Pa tsiku la 8 muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzipereka nsembe yowotcha pamoto kwa Yehova. Umenewu ndi msonkhano wapadera. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.

  • Deuteronomo 16:13-15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Muzichita Chikondwerero cha Misasa+ kwa masiku 7, mukamatuta zokolola kuchokera pamalo opunthira mbewu, pamalo oyengera mafuta ndi pamalo opondera mphesa. 14 Muzisangalala pa chikondwerero chimenecho,+ inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali mumzinda wanu. 15 Muzichitira Yehova Mulungu wanu chikondwerero chimenecho kwa masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Muzichita chikondwererochi chifukwa Yehova Mulungu wanu adzadalitsa zokolola zanu zonse ndi chilichonse chimene dzanja lanu likuchita,+ ndipo inu mudzakhala osangalala kwambiri.+

  • Nehemiya 8:14-18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndiyeno anapeza kuti mʼChilamulo chimene Yehova anawapatsa kudzera mwa Mose analembamo kuti Aisiraeli azikhala mʼmisasa pa nthawi yachikondwerero mʼmwezi wa 7.+ 15 Analembamonso kuti azilengeza mofuula+ mʼmizinda yonse ndi ku Yerusalemu konse kuti: “Pitani kumapiri mukatenge nthambi za mitengo ya maolivi, nthambi za mitengo ya paini, nthambi za mitengo ya mchisu, mitengo ya kanjedza ndi nthambi za masamba ambiri za mitengo ina kuti mudzamangire misasa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.”

      16 Choncho anthu anapita nʼkukatenga zinthu zimenezi ndipo anamangira misasa. Aliyense anamanga msasa pamwamba pa nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu woona,+ mʼbwalo lalikulu la Geti la Kumadzi+ ndiponso mʼbwalo lalikulu la Geti la Efuraimu.+ 17 Choncho gulu lonse la anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo anamanga misasa nʼkukhala mʼmisasayo. Anthu anasangalala kwambiri+ chifukwa Aisiraeli anali asanachitepo zimenezi kuchokera mu nthawi ya Yoswa+ mwana wa Nuni, mpaka nthawi imeneyi. 18 Ndiyeno tsiku lililonse, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, ankawerenga mokweza buku la Chilamulo cha Mulungu woona.+ Anachita chikondwererochi masiku 7 ndipo pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera mogwirizana ndi Chilamulo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena