-
Numeri 18:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Utengenso abale ako a fuko la Levi, omwe ndi a mtundu wa bambo ako, kuti azikuthandiza. Azitumikira iweyo+ limodzi ndi ana ako pachihema cha Umboni.+ 3 Azichita utumiki umene mwawapatsa komanso azigwira ntchito zawo zonse zapachihema.+ Koma asamayandikire zipangizo zamʼmalo oyera, kapena kuyandikira guwa lansembe kuti iwowo kapena inuyo musafe.+
-
-
1 Mbiri 23:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Ana a Leviwa analinso ndi udindo wokhudza chihema chokumanako, malo oyera ndiponso abale awo, omwe anali ana a Aroni, pa utumiki wapanyumba ya Yehova.
-