-
Numeri 4:34-36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Kenako Mose ndi Aroni pamodzi ndi atsogoleri+ a anthuwo, anawerenga ana a Kohati+ potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo. 35 Anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito pachihema chokumanako.+ 36 Onse amene anawerengedwa, mogwirizana ndi mabanja awo, anakwana 2,750.+
-