27 Mabanja a Aamuramu, Aizara, Aheburoni ndi Auziyeli anachokera mwa Kohati.+ Amenewa ndi amene anali mabanja a Akohati. 28 Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, analipo 8,600. Amenewa ntchito yawo inali kutumikira pamalo oyera.+