Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 27:1-7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Kenako ana aakazi a Tselofekadi+ anafika kwa Mose. Tselofekadi anali mwana wa Heferi, Heferi anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Makiri ndipo Makiri anali mwana wa Manase. Onsewa anali ochokera kumabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana aakazi a Tselofekadi amenewa mayina awo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 2 Iwo anakaimirira pamaso pa Mose, wansembe Eleazara, atsogoleri+ komanso gulu lonse, pakhomo la chihema chokumanako nʼkunena kuti: 3 “Bambo athu anafera mʼchipululu. Koma iwo sanali mʼgulu la anthu amene ankatsatira Kora,+ omwe anasonkhana kuti atsutsane ndi Yehova. Bambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo, ndipo analibe mwana aliyense wamwamuna. 4 Kodi dzina la bambo athu lisapezekenso ku banja lawo chifukwa chakuti analibe mwana wamwamuna? Chonde, tipatseni cholowa pakati pa azichimwene a bambo athu.” 5 Choncho Mose anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.+

      6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 7 “Ana aakazi a Tselofekadi akunena zoona. Uwapatsedi malo kuti akhale cholowa chawo pakati pa azichimwene a bambo awo. Cholowa cha bambo awocho chikhale chawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena