Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 5:11, 12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Koma ngati sangakwanitse kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ kuti ukhale nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lake. Asauthire mafuta ndipo asaikemo lubani chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo. 12 Akatero azibweretsa ufawo kwa wansembe, ndipo wansembeyo autape kudzaza dzanja limodzi kuimira nsembe yonseyo. Kenako auwotche paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yamachimo.

  • Levitiko 6:25, 26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Ili ndi lamulo la nsembe yamachimo:+ Pamalo amene mukuphera nyama ya nsembe yopsereza+ muzipheraponso nyama ya nsembe yamachimo pamaso pa Yehova. Nsembeyi ndi yopatulika koposa. 26 Wansembe amene waipereka monga nsembe yamachimo aziidya.+ Aziidyera kumalo oyera, mʼbwalo la chihema chokumanako.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena