-
Numeri 24:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako Balaki anapsera mtima Balamu. Ndiyeno Balaki anawomba mʼmanja mokwiya nʼkuuza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere adani anga,+ koma iwe wawadalitsa kwambiri maulendo atatu onsewa. 11 Nyamuka pompano uzipita kwanu. Ine ndimafuna ndikupatse mphoto,+ koma taona! Yehova wakulepheretsa kulandira mphoto.”
-