28 Choncho Balaki anatenga Balamu nʼkupita naye pamwamba pa phiri la Peori, limene linayangʼanizana ndi Yesimoni.+ 29 Kenako Balamu anauza Balaki kuti: “Mumange maguwa ansembe 7 pamalo ano ndipo mundikonzere ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.”+