-
Numeri 16:39, 40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Choncho wansembe Eleazara anatenga zofukizira zakopa zimene anthu amene anapsa ndi moto aja anabweretsa, ndipo anazisula nʼkupanga timalata tokutira guwa lansembe, 40 mogwirizana ndi zimene Yehova anamuuza kudzera mwa Mose. Timalatato tinali chikumbutso kwa Aisiraeli kuti munthu wamba* amene si mbadwa ya Aroni asayandikire kwa Yehova kuti akapereke nsembe zofukiza.+ Anachita zimenezi kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi anthu amene ankamutsatira anachita.+
-
-
2 Mbiri 26:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Iwo anapita pamene panali Mfumu Uziya kukamuletsa. Anamuuza kuti: “Mfumu Uziya, si zoyenera kuti inuyo mupereke nsembe zofukiza kwa Yehova.+ Ansembe okha ndi amene ayenera kupereka nsembe zofukiza chifukwa ndi mbadwa za Aroni+ ndipo anayeretsedwa. Tulukani mʼnyumba yopatulikayi popeza mwachita zosakhulupirika ndipo zimenezi sizikubweretserani ulemerero wochokera kwa Yehova Mulungu.”
-