34Kenako Mose anachoka mʼchipululu cha Mowabu kupita mʼphiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyangʼanizana ndi Yeriko.+ Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+
4 Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Ili ndi dziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzalipereka kwa mbadwa* zanu.’+ Ndakulola kuti ulione ndi maso ako, koma suwoloka kukalowa mʼdzikolo.”+