Numeri 18:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa mʼdziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa malo pakati pawo kuti akhale cholowa chako.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisiraeli.+ Numeri 18:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Chakhumi chimene Aisiraeli azipereka kwa Yehova, ndapereka kwa Alevi kuti chikhale cholowa chawo. Nʼchifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa Aisiraeli.’”+ Deuteronomo 18:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 “Alevi omwe ndi ansembe, komanso fuko lonse la Levi, sadzapatsidwa gawo kapena cholowa pakati pa Aisiraeli. Iwo azidzadya nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, zomwe ndi cholowa chake.+
20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa mʼdziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa malo pakati pawo kuti akhale cholowa chako.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisiraeli.+
24 Chakhumi chimene Aisiraeli azipereka kwa Yehova, ndapereka kwa Alevi kuti chikhale cholowa chawo. Nʼchifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa Aisiraeli.’”+
18 “Alevi omwe ndi ansembe, komanso fuko lonse la Levi, sadzapatsidwa gawo kapena cholowa pakati pa Aisiraeli. Iwo azidzadya nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, zomwe ndi cholowa chake.+