29 Mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ 30 Nonsenu simudzalowa mʼdziko limene ndinalumbira kuti mudzakhalamo,+ kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+