-
Yoswa 10:36, 37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
36 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anachoka ku Egiloni nʼkupita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Heburoni.+ 37 Analanda mzindawo ndipo anapha ndi lupanga mfumu yake, anthu ake onse komanso anthu amʼmidzi yake yonse. Anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Choncho anawononga mzindawo ndi aliyense amene anali mmenemo ngati mmene anachitira ku Egiloni.
-