27 Pamapeto pake Yakobo anafika kwa bambo ake Isaki ku Mamure,+ mʼdera la Kiriyati-ariba, komwe ndi ku Heburoni. Uku nʼkumenenso Abulahamu ndi Isaki anakhalako monga alendo.+
11 Anawapatsa Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali bambo wa Anaki.) Mzindawu pamodzi ndi malo ouzungulira odyetserako ziweto unali mʼdera lamapiri la Yuda. 12 Koma malo ena onse amumzindawo komanso midzi yake, anawapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune kuti akhale ake.+