-
Oweruza 13:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Manowa anachonderera Yehova kuti: “Yehova, tikupempha kuti munthu wa Mulungu woona amene munamutuma uja, abwerenso kuti adzatilangize zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.” 9 Mulungu woona anamva zimene Manowa anapempha, moti mngelo wa Mulungu woona uja anabweranso kwa mkaziyo, ndipo anamʼpeza atakhala pansi panja. Pa nthawiyi sanali limodzi ndi mwamuna wake Manowa.
-