-
Yoswa 5:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima patsogolo pake, atanyamula lupanga mʼmanja.+ Yoswa anamuyandikira nʼkumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?” 14 Munthuyo anayankha kuti: “Ayi, ndabwera chifukwa ndine kalonga* wa gulu lankhondo la Yehova.”+ Atatero, Yoswa anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamuuza kuti: “Lankhulani mbuyanga kwa kapolo wanu.”
-