Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 19:4, 5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Koma iwo asanagone, chigulu cha amuna a mumzinda wa Sodomu, chinafika nʼkuzungulira nyumba ya Loti. Pachigulupo panali anyamata komanso achikulire. 5 Iwo ankauza Loti mofuula kuti: “Kwanu kuno kwabwera amuna enaake usiku uno. Ali kuti amuna amenewo? Atulutse kuti tigone nawo.”+

  • Levitiko 20:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Mwamuna akagona ndi mwamuna mnzake ngati mmene mwamuna amagonera ndi mkazi, onse awiri achita chinthu chonyansa.+ Iwo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo uzikhala pa iwo.

  • Aroma 1:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi nʼkumatenthetsana okhaokha mwachiwawa ndi chilakolako choipa, amuna okhaokha+ kuchitirana zonyansa nʼkulandiriratu mphoto yoyenerera kulakwa kwawo.+

  • 1 Akorinto 6:9, 10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu?+ Musapusitsidwe.* Achiwerewere,*+ olambira mafano,+ achigololo,+ amuna amene amalola kugonedwa ndi amuna anzawo,+ amuna ogona amuna anzawo,+ 10 akuba, adyera,+ zidakwa,+ olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.+

  • Yuda 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Mofanana ndi zimenezi, anthu amʼmizinda ya Sodomu ndi Gomora komanso mizinda yozungulira ankachita chiwerewere* chonyansa kwambiri ndiponso kugonana mʼnjira imene si yachibadwa.+ Anthu amenewa anapatsidwa chilango cha chiwonongeko chosatha*+ ndipo ndi chitsanzo chotichenjeza.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena