Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 33:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 Koma ngati simukathamangitsa anthu amene akukhala mʼdzikolo,+ anthu amene mukawasiyewo adzakhala ngati zitsotso mʼmaso mwanu, ndiponso ngati minga yokubayani mʼnthiti mwanu. Ndipo iwo azidzakuvutitsani mʼdziko limene muzidzakhala.+

  • Deuteronomo 8:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Muzikumbukira njira yaitali imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani mʼchipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani mʼchipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa komanso kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mungasunge malamulo ake kapena ayi.

  • Yoswa 23:12, 13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Koma mukasiya Mulungu nʼkumamatira anthu a mitundu ina, amene atsala pakati panuwa+ nʼkumakwatirana nawo+ komanso kumagwirizana nawo, 13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzasiya kuwathamangitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu. Adzakhalanso ngati zikwapu kumsana kwanu+ komanso ngati zitsotso mʼmaso mwanu, mpaka mutatheratu mʼdziko labwino limene Yehova Mulungu wanu wakupatsanili.

  • Oweruza 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mulungu anagwiritsa ntchito mitunduyi poyesa Aisiraeli kuti aone ngati adzamvere malamulo amene Yehova anapereka kwa makolo awo kudzera mwa Mose.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena