-
Ekisodo 23:31-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Dziko limene ndidzakupatsani lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita zimenezi chifukwa anthu okhala mʼdzikomo ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo inu mudzawathamangitsa pamaso panu.+ 32 Musamachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo.+ 33 Asamakhale mʼdziko lanu kuti asakuchititseni kuti mundichimwire. Mukadzatumikira milungu yawo, udzakhala msampha ndithu kwa inu.”+
-
-
Deuteronomo 7:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Musadzachite nawo mgwirizano uliwonse wa ukwati.* Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna ndipo musadzatenge ana awo aakazi nʼkuwapereka kwa ana anu aamuna.+ 4 Chifukwa adzachititsa kuti ana anu aamuna asiye kunditsatira ndipo adzatumikira milungu ina.+ Ndiyeno mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani mofulumira.+
-
-
Yoswa 23:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Koma mukasiya Mulungu nʼkumamatira anthu a mitundu ina, amene atsala pakati panuwa+ nʼkumakwatirana nawo+ komanso kumagwirizana nawo, 13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzasiya kuwathamangitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu. Adzakhalanso ngati zikwapu kumsana kwanu+ komanso ngati zitsotso mʼmaso mwanu, mpaka mutatheratu mʼdziko labwino limene Yehova Mulungu wanu wakupatsanili.
-
-
Oweruza 2:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Inuyo musachite pangano ndi anthu okhala mʼdzikoli,+ ndipo mugwetse maguwa awo ansembe.’+ Koma inu simunamvere mawu anga.+ Nʼchifukwa chiyani mwachita zimenezi? 3 Nʼchifukwa chake ndinanena kuti, ‘Sindidzawathamangitsa pamaso panu,+ koma adzakhala msampha wanu,+ ndipo milungu yawo idzakhala ngati nyambo.’”+
-