25 Pa nthawi imene Aisiraeli ankakhala ku Sitimu,+ anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.+ 2 Akaziwo anaitana Aisiraeliwo kuti azikapereka nsembe kwa milungu yawo+ ndipo Aisiraeliwo anayamba kudya nsembezo komanso kugwadira milungu ya Amowabu.+