-
1 Samueli 6:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mukatero, mutenge Likasa la Yehova nʼkuliika mungoloyo. Ndiyeno mutenge zinthu zagolide zimene mukuzitumiza ngati nsembe yakupalamula nʼkuizika mʼbokosi lina pambali pa Likasalo,+ kenako mulitumize lizipita. 9 Ndiyeno muzikaliyangʼana: Likasalo likakalowera njira yopita kwawo ku Beti-semesi,+ ndiye kuti iye ndi amenedi watichitira zinthu zoipa kwambirizi. Koma ngati silikalowera kumeneko, tidzadziwa kuti si dzanja lake limene latichitira zoipazi, koma zangochitika.”
-