-
1 Samueli 6:21-7:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Kenako anatumiza uthenga kwa anthu a ku Kiriyati-yearimu+ wakuti: “Afilisiti abweza Likasa la Yehova, bwerani mudzalitenge.”+
7 Choncho amuna a ku Kiriyati-yearimu anabweradi nʼkutenga Likasa la Yehova ndipo anakaliika mʼnyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Ndiyeno anasankha* Eliezara mwana wake kuti azilondera Likasa la Yehova.
-
-
2 Samueli 6:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Davide anasonkhanitsanso asilikali amphamvu mu Isiraeli, okwana 30,000. 2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka nʼkupita ku Baale-yuda kuti akatenge Likasa la Mulungu woona.+ Pa likasa limeneli anthu amaitanirapo dzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+
-