7 Davide atamva zimenezi anatumiza Yowabu ndi gulu lonse lankhondo, limodzinso ndi asilikali ake amphamvu.+ 8 Ndiyeno Aamoni anapita kukaima pageti la mzinda atakonzekera kumenya nkhondo. Pomwe Asiriya a ku Zoba, a ku Rehobu, a ku Isitobu ndi a ku Maaka anakayalana kwaokha kutchire.