-
2 Samueli 10:9-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Yowabu ataona kuti adani ake akubwera kuchokera kutsogolo ndi kumbuyo, anasankha ena mwa magulu a asilikali amphamvu mu Isiraeli nʼkuwakonzekeretsa kuti amenyane ndi Asiriya.+ 10 Anthu ena onse anawapereka kwa mchimwene wake Abisai+ kuti awatsogolere pokamenyana ndi Aamoni.+ 11 Ndiyeno anamuuza kuti: “Ukaona kuti Asiriya akundigonjetsa, ubwere udzandipulumutse. Koma Aamoni akayamba kukugonjetsa, ineyo ndibwera kudzakupulumutsa. 12 Tikuyenera kuchita zinthu mwamphamvu komanso molimba mtima+ chifukwa cha anthu athu ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Yehova adzachita zimene akuona kuti nʼzabwino kwa iye.”+
-