-
1 Mbiri 29:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Komanso chifukwa chakuti ndikusangalala ndi nyumba ya Mulungu wanga,+ kuwonjezera pa zonse zimene ndakonzekera zokhudza nyumba yopatulikayo, ndikupereka kunyumba ya Mulungu wanga chuma changa+ chomwe ndi golide ndi siliva. 4 Ndikupereka matalente* 3,000 a golide wa ku Ofiri,+ matalente 7,000 a siliva woyengedwa bwino wodzakutira makoma a nyumba,
-