19 Yosiya anachotsanso akachisi onse a mʼmalo okwezeka amene anali mʼmizinda ya ku Samariya,+ omwe mafumu a Isiraeli anamanga kuti akwiyitse Mulungu. Zimene anachita ndi akachisiwa zinali zofanana ndi zimene anachita ku Beteli.+
30Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembera makalata anthu a ku Efuraimu ndi ku Manase+ kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzachitira Pasika Yehova Mulungu wa Isiraeli.+