33 Kataniyi uipachike mʼmunsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la Umboni+ kuseri kwa kataniyi. Kataniyi ikhale malire a Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+
6 Kenako ansembe anabweretsa likasa la pangano la Yehova pamalo ake,+ kuchipinda chamkati cha nyumbayo, chomwe ndi Malo Oyera Koposa, ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+
24 Khristu sanalowe mʼmalo oyera opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu mʼmalo mwa ifeyo.+