Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 40:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Atatero analowetsa Likasa mʼchihema nʼkuika katani+ pamalo ake ndipo inatchinga likasa la Umboni,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

  • Levitiko 16:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni mʼbale wako kuti asamalowe mʼmalo oyera+ kuseri kwa katani,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, pa nthawi iliyonse imene wafuna, kuopera kuti angafe+ chifukwa ine ndidzaonekera mumtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+

  • 1 Mafumu 8:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kenako ansembe anabweretsa likasa la pangano la Yehova pamalo ake,+ kuchipinda chamkati cha nyumbayo, chomwe ndi Malo Oyera Koposa, ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+

  • Aheberi 9:2-4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Chifukwa panamangidwa chipinda choyamba cha chihema ndipo mʼchipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo ndi mikate yoonetsa kwa Mulungu,*+ ndipo chinkatchedwa “Malo Oyera.”+ 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+ 4 Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe+ ndi likasa la pangano+ lokutidwa ndi golide.+ Mulikasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana,+ ndodo ya Aroni imene inaphuka ija+ komanso miyala yosema+ ya pangano.

  • Aheberi 9:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iye analowa mʼmalo oyera ndi magazi ake,+ osati ndi magazi a mbuzi kapena a ngʼombe zazingʼono zamphongo. Analowa kamodzi kokha mʼmalo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya.+

  • Aheberi 9:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Khristu sanalowe mʼmalo oyera opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu mʼmalo mwa ifeyo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena