10 Mupange likasa la mtengo wa mthethe, masentimita 110 mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+ 11 Kenako mulikute ndi golide woyenga bwino.+ Mkati ndi kunja komwe mulikute ndi golide, ndipo mupange mkombero wagolide kuzungulira likasalo.+