-
Ekisodo 37:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Kenako Bezaleli+ anapanga Likasa+ la mtengo wa mthethe masentimita 110* mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+ 2 Analikuta ndi golide woyenga bwino mkati ndi kunja komwe ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+ 3 Ndiyeno analipangira mphete 4 zagolide zoika pamwamba pa miyendo yake 4. Mphete ziwiri zinali mbali imodzi ndipo mphete zina ziwiri zinali mbali inayo. 4 Anapanganso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide.+ 5 Kenako analowetsa ndodo zonyamulirazo mumphete zamʼmbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo.+
-