-
Ekisodo 25:10-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Mupange likasa* la mtengo wa mthethe, masentimita 110* mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+ 11 Kenako mulikute ndi golide woyenga bwino.+ Mkati ndi kunja komwe mulikute ndi golide, ndipo mupange mkombero wagolide kuzungulira likasalo.+ 12 Mulipangire mphete 4 zagolide ndi kuziika pamwamba pa miyendo yake 4. Mphete ziwiri zikhale mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zikhale mbali inayo. 13 Mupangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe nʼkuzikuta ndi golide.+ 14 Mulowetse ndodo zonyamulirazo mumphete zamʼmbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo. 15 Ndodo zonyamulirazo zizidzakhala mumphete za Likasalo. Sizikuyenera kuchotsedwamo.+
-