-
Nehemiya 2:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako ndinawauza kuti: “Inu mukuona vuto lalikulu limene tili nalo. Yerusalemu ndi bwinja ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto. Tiyeni timangenso mpanda wa Yerusalemu kuti anthu asiye kutinyoza.”
-
-
Danieli 9:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene lamulo lakuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso+ lidzaperekedwe kukafika pamene Mesiya*+ Mtsogoleri+ adzaonekere, padzadutsa milungu 7 komanso milungu 62.+ Yerusalemu adzakonzedwa ndi kumangidwanso ndipo adzakhala ndi bwalo ndi ngalande yachitetezo. Koma zimenezi zidzachitika pa nthawi ya mavuto.
-