2 Mofanana ndi mphepo imene imathamangitsa utsi, inunso muwathamangitsire kutali.
Mofanana ndi phula limene limasungunuka pamoto,
Anthu oipa awonongeke pamaso pa Mulungu.+
3 Koma olungama asangalale,+
Asangalale kwambiri pamaso pa Mulungu,
Adumphe ndi chisangalalo.