-
1 Samueli 30:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Koma Davide anati: “Ayi abale anga, musatero ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watiteteza ndiponso wapereka mʼmanja mwathu gulu la achifwamba limene linadzatiukira.+ 24 Ndani angavomereze zimenezo? Zomwe alandire munthu amene anapita kunkhondo, zikhala zofanana ndi zimene alandire munthu amene amalondera katundu.+ Aliyense alandirapo kenakake.”+ 25 Ndipo kuyambira tsiku limenelo, iye anaonetsetsa kuti limeneli likhale lamulo loti Aisiraeli azitsatira mpaka lero.
-