-
Salimo 40:13-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Mukhale wofunitsitsa kundipulumutsa, inu Yehova.+
Ndithandizeni mofulumira, inu Yehova.+
14 Onse amene akufuna kuchotsa moyo wanga
Achititsidwe manyazi komanso anyozeke.
Amene akusangalala ndi tsoka langa
Abwerere mwamanyazi.
15 Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”
Achite mantha kwambiri chifukwa cha zinthu zochititsa manyazi zimene ziwachitikire.
Amene amasangalala ndi njira imene mumapulumutsira anthu, nthawi zonse azinena kuti:
“Yehova alemekezeke.”+
17 Koma ine ndine munthu wovutika komanso wosauka.
Yehova aone zimene zikundichitikira.
-