-
Genesis 45:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndiyeno Yosefe anauza abale akewo kuti: “Sunthirani pafupi ndi ine.” Ndipo anasunthiradi pafupi ndi iye.
Kenako Yosefe anati: “Ndine mʼbale wanu uja Yosefe, amene munamugulitsa ku Iguputo.+ 5 Koma musadzimvere chisoni kapena kuimbana mlandu kuti munandigulitsa kuno, chifukwa Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti tikhalebe ndi moyo.+
-