-
Numeri 25:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 “Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, wabweza mkwiyo wanga pa Aisiraeli, chifukwa sanalekerere ngakhale pangʼono kuti anthu azipikisana nane pakati pawo.+ Choncho sindinawononge Aisiraeliwa, ngakhale kuti ndimafuna kuti anthu azikhala odzipereka kwa ine ndekha.+ 12 Pa chifukwa chimenechi, umuuze Pinihasi kuti, ‘Ndikupangana naye pangano la mtendere. 13 Limeneli likhala pangano la unsembe kwa iye ndi mbadwa zake mpaka kalekale,+ chifukwa sanalekerere zoti anthu azipikisana ndi Mulungu wake+ ndiponso anaphimba machimo a Aisiraeli.’”
-