-
Deuteronomo 17:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Akakhala pampando wachifumu, ayenera kukopera buku lakelake la Chilamulo ichi, kuchokera mʼbuku limene* Alevi omwe ndi ansembe amasunga.+
19 Buku limeneli azikhala nalo nthawi zonse ndipo aziliwerenga masiku onse a moyo wake,+ kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake ndi kusunga mawu onse a Chilamulo ichi, komanso kutsatira malangizo ake.+ 20 Akachita zimenezi sadzadzikweza pamaso pa abale ake, komanso sadzachoka pachilamulo nʼkupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere, kuti iyeyo ndi ana ake apitirize kukhala mafumu mu Isiraeli kwa nthawi yaitali.”
-