19 ndiye ndidzadziuza kuti: “Uli ndi zinthu zambiri zabwino ndipo zisungika kwa zaka zambiri. Mtima mʼmalo, udye, umwe ndi kusangalala.”’ 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako aufuna. Nanga zinthu zimene wasungazi zidzakhala za ndani?’+