1 Wosangalala ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,
Saima mʼnjira ya anthu ochimwa,+
Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+
2 Koma amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova,+
Ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama chilamulocho masana ndi usiku.+