-
Mateyu 4:13-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Kenako atachoka ku Nazareti, anafika ku Kaperenao+ nʼkupeza malo okhala mʼmbali mwa nyanja mʼzigawo za Zebuloni ndi Nafitali, 14 kuti mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya akwaniritsidwe. Iye ananena kuti: 15 “Anthu amene akukhala mʼdziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, mʼmbali mwa msewu wakunyanja kutsidya lina la Yorodano, ku Galileya kumene kunkakhala anthu a mitundu ina, 16 anthu amene ankakhala mumdima anaona kuwala kwakukulu, ndipo anthu amene ankakhala mʼdera lamthunzi wa imfa, kuwala+ kunawaunikira.”+
-