-
Yoswa 13:15-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kenako Mose anagawira cholowa fuko la Rubeni motsatira mabanja awo. 16 Dera lawo linayambira ku Aroweli, mzinda umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho komanso malo onse okwera a Medeba. 17 Linafikanso ku Hesiboni ndi midzi yake yonse+ imene inali mʼmalo okwera, ku Diboni, ku Bamoti-baala komanso ku Beti-baala-meoni.+
-