-
Yesaya 20:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Kenako Yehova anati: “Mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu, kuti akhale chizindikiro+ ndi chenjezo kwa Iguputo+ ndi Itiyopiya.+ 4 Mofanana ndi zimenezi, mfumu ya Asuri idzagwira gulu la anthu ku Iguputo+ ndi ku Itiyopiya nʼkupita nawo ku ukapolo kudziko lina. Idzagwira anyamata ndi amuna achikulire, ali opanda zovala ndi opanda nsapato, ndiponso matako awo ali pamtunda moti Iguputo adzachititsidwa manyazi.
-
-
Yeremiya 43:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndikuitana Nebukadinezara* mfumu ya Babulo mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala imene ndaibisayi. Iye adzamanga tenti yake yachifumu pamwamba pa miyala imeneyi.+ 11 Nebukadinezara adzabwera nʼkuukira dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo ndipo woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+
-