Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti:

      “Bwerani. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova,

      Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+

      Iye akatiphunzitsa njira zake,

      Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”+

      Chifukwa chilamulo chidzaphunzitsidwa* mu Ziyoni,

      Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.+

  • Yesaya 25:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Mʼphiri ili,+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakonzera anthu a mitundu yonse,

      Phwando la zakudya zabwino kwambiri,+

      Phwando la vinyo wabwino kwambiri,*

      Phwando la zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta amʼmafupa,

      Ndiponso la vinyo wabwino kwambiri, wosefedwa bwino.

  • Yesaya 52:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 52 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu+ iwe Ziyoni.+

      Vala zovala zako zokongola+ iwe Yerusalemu, mzinda woyera.

      Chifukwa munthu wosadulidwa ndi wodetsedwa sadzabweranso mwa iwe.+

  • Yeremiya 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pa nthawi imeneyo mzinda wa Yerusalemu adzautchula kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsa pamodzi ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso khosi nʼkumatsatira mitima yawo yoipayo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena