20 Yehova akuyankheni pa tsiku la mavuto.
Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+
2 Akutumizireni thandizo kuchokera kumalo ake opatulika+
Ndipo akuthandizeni ali ku Ziyoni.+
3 Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.
Alandire mosangalala nsembe zanu zopsereza. (Selah)