-
Yeremiya 21:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 ‘Yehova wanena kuti: “Kenako Zedekiya mfumu ya Yuda, atumiki ake ndi anthu amumzindawu, onse amene adzapulumuke ku mliri, lupanga ndi njala yaikulu, ndidzawapereka mʼmanja mwa Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo. Ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo komanso mʼmanja mwa amene akufuna kuchotsa moyo wawo.+ Nebukadinezara adzawapha ndi lupanga ndipo sadzawamvera chisoni, kuwakomera mtima kapena kuwachitira chifundo.”’+
-
-
Yeremiya 34:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndipo izi ndi zimene zidzachitikire anthu amene anaphwanya pangano langa posatsatira mawu a mʼpangano limene iwo anachita pamaso panga. Iwo anachita pangano limeneli podula mwana wa ngʼombe pakati nʼkudutsa pakati pa mbali ziwirizo.+ 19 Anthuwa ndi akalonga a Yuda, akalonga a Yerusalemu, nduna zapanyumba ya mfumu, ansembe ndi anthu onse amʼdzikoli amene anadutsa pakati pa mwana wa ngʼombe yemwe anamudula pakati. 20 Ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo ndi mʼmanja mwa onse amene akufuna moyo wawo. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zouluka mumlengalenga ndi zilombo zakutchire.+
-