-
2 Mbiri 34:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya, Ahikamu+ mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi ndi Asaya mtumiki wa mfumu, kuti: 21 “Pitani mukafunsire kwa Yehova mʼmalo mwa ineyo ndiponso mʼmalo mwa anthu amene atsala mu Isiraeli ndi mu Yuda. Mukafunse zokhudza mawu amʼbuku limene lapezekali, chifukwa mkwiyo umene Yehova adzatisonyeze ndi waukulu, popeza makolo athu sanasunge mawu a Yehova moti sanatsatire zonse zimene zinalembedwa mʼbukuli.”+
-